Khoti lichosa mulandu umodzi pa milandu iwiri yomwe akuzenga a Dalitso Kabambe: Akuti boma lilibe umboni

Bwalo lalikulu la milandu ku Lilongwe lathetsa umodzi mwa milandu yomwe mkulu wakale wa banki ya Reserve a Dalitso Kabambe ndi wachiwiri wao a Henry Mathanga akhala akuyankha okhudza kuganiziridwa kuti ankanamiza bungwe lopereka ngongole la International Monetary Fund.

Dr Dalitso Kabambe

Malingana ndi chigamulo chomwe apereka oweruza a Redson Kapindu, mulandu omwe wathetsedwa ndi oti awiriwa anagwiritsa ntchito udindo awo molakwika.

Kuthetsedwa kwa mlanduwu akuti kwadza chifukwa chakuti boma lakanika kuimba anthuwa mlanduwu mu miyezi khumi ndi iwiri monga mmene amanenela malamulo osanthula za milandu ya ikulu ikulu. (Criminal Procedure and Evidence Code)

Ndime 302A(1) ya malamulowa, chigamulocho chomwe chinaperekedwa lachisanu lapitali chati, milandu yomwe chilango chake sichimapitilira zaka zitatu, monga ogwiritsa ntchito udindo molakwikawu, umayenera kuzengedwa miyezi khumi ndi iwiri.

Koma boma silinakwanitse izi ngakhale kuti linamanga awiriwa zaka zitatu zapitazo, bwalolo linatero.

A Kabambe ndi a Mathanga anapemphanso bwaloli kuti lithetse mlandu wa chiwiri oti iwowa anachita zachinyengo.

Oweruzawa anati adikire kaye kuti mlanduwu adzayambe kaye kuuzenga.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
State revives Mwanamveka’s 2021 case: Commits him to High Court for formal charging

In an interesting twist to the justice tale, the State, through the Director of Public Prosecutions (DPP), Masauko Chamkakala, has...

Close