Konveshoni ya MCP yapsa pa 10 August: Koma anenetsa kuti obwera kumene muchipani sakapisana nawo

Wapampando wamsonkhano waukulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Kezzie Msukwa watsimikizira atolankhani kum’mawaku ku Lilongwe kuti ganizo la chipanichi loletsa aliyese kuima pamipando yemwe wangolowa kumene ndipo sadathe zaka ziwiri likadalipo.

A Msukwa kuyankhula pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe

A Msukwa anenetsa kuti izi zili motere pofuna kusunga umwini wa chipani. Iwo anenetsa kuti kwina kulikonse kumakhala ndondomeko zosankhira adindo ake m’mipando.

Mukulankhula kwawo a Msukwa awuza msonkhano wa atolankhani kuti zonse zokonzekera mwambowu zikuyenda bwino. A Msukwa ati mwambowu ukachitikira ku Bingu International Conference Centre (BICC) kuyambira pa 8 mpaka10 August , 2024.

Malingana ndi a Kezzie Msukwa onse omwe akufuna mipando ku chipanichi apemphedwa kuyamba kukatenga ma zikalata ku ofesi ya chipanichi komanso mumaofesi wena ammadera. A Msukwa ati kumeneku onse obwela alibe mwayi oyima nawo pampando ulionse pokha pokha iwo atakwanitsa zaka ziwiri ali mchipani onse ofuna kukatenga dzikalata atha kutero kuyambira pa 1 July, kulekeza pa 24 July , 2024.

Malingana ndi a Msukwa , yemwe akufuna kuima pampando wa mkulu wa chipanichi kapena kuti mpando wa utsogoleri akuyenera kukapereka ndalama zokwana K5Million. Malingana ndi a Msukwa yemwe akupikisaka ngati wachiwiri kwa mtsogoleri oyamba ndi wachiwiri wake akuyembekezeka kupereka ndalama zokwana K2.5Million.

A Msukwa anenetsa kuti yemwe akufuna mpando wa mlembi wamkulu akuyembekezeka kulipira ndalama zokwana K2Million. Adzitsogoleri munthambi zosiyanasiyana mchipanichi akuyenera kupereka ndalama zokwana K500, 000. Achinyamata ndi azimai adzapereka theka la ndalama.

M’modzi mwa akuluakulu ku bungwe lokonzekera mwambowu, a Joseph Njobvuyalema apempha omwe akufuna mipando kuti atha kukaponya ndalama zawo ku Bank ya NBS yomwe number yake ndi 24379779

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Exclusive: Chilima autopsy reveals that he died due to massive impact of the plane crash

Former vice president Dr Saulos Chilima died due to severe and extensive injuries caused by the massive impact of the...

Close