Kukoma Ntopwa yalandira thandizo la K10 miliyoni
Kampani ya Capital Oil Refining Industries (Cori) yathandiza timu yampira wamiyendo koma osewera ake ali akazi ya Kukoma Ntopwa ndi ndalama zokwana 10 miliyoni Kwacha kuti zithandizire timuyi pamene ikukachita nawo mpikisano wa chaka chino wa COSAFA womwenso ukathandizire kupeza matimu oti alowe nawo mu mpikisano wa CAF Women’s Champions League.

Timuyi inyamuka kupita ku mpikisanowu sabata yomwe ino ndipo mpikisanowu ukachitikira mu mzinda wa Johannesburg m’dziko la South Africa kuyambira pa 22 mpaka pa 31 August.
Mkulu woyang’ana za zithandizo zosiyanasiyana ku kampani ya Cori a Violet Kapolo ati anaganiza zothandiza timuyi ngati njira imodzi yopereka mangolomera kwa osewera kuti akachite bwino ku mpikisanowu.
“Tili ndi udindo owonetsetsa kuti timuyi ndiyolimbikitsidwa pamene ikupita ku mpikisano woterewu. Iwowatu anyamula mbendera ya Malawi ndipo tikuyembekezera kuti akakhala chitsanzo chabwino komanso akakhala osunga mwambo ku mpikisanowu,” anayankhula choncho a Kapolo.
Mkulu wa timuyi a Isaac Jomo Osman ayamikira kampaniyi kaamba ka thandizoli.
“Ndife okondwa chifukwa choti atipatsa ndalama zowonjezera kuti tikwanitse kupita ku South Africa. Tili ndi chikhulupiliro kuti tikachita bwino ku mpikisanowu komwe tikukayimilira dziko lino,” atero a Osman.
Timu ya Ntopwa ikasewera masewero ake oyamba ndi timu ya Mamelodi Sundowns ya ku South Africa pabwalo la UJ AW Muller Lachisanu pa 22 August ndipo pa 24 August ikasewera masewero ake achiwiri ndi timu ya Beauties ya ku Namibia. Masewero otsiriza a timuyi mu Gulu A adzakhalapo pa 26 August ndi timu ya Zesco Ndola Girls yochokera m’dziko la Zambia.
Matimu opambana m’magulu mwawo akapitilira mu ndime ya semi finals.
Follow and Subscribe Nyasa TV :