Kwanunkha ku Joni: A Malawi enanso 250 achokochedwako, afika mawa mdziko muno
A Malawi okwana 210 omwe athamangitsidwa m’dziko la South Africa akuyembekezereka kufika m’dziko muno mawa.
Anthuwa akwanitsa chiwerengero cha anthu omwe athamangitsidwa m’dzikolo mwezi uno kufika pa 490 Kamba koti nzika zina zokwana 280 zinafika m’dziko muno kudzera pa chipata cha boma la Mwanza, sabata yatha.
M’neneri wa nthambi yoona za anthu olowa ndi kuturuka m’dziko muno , Wellington Chiponde watsimikiza za izi ndipo wati anthuwa akukhudzidwa ndi milandu yosinasiyana yokhudza kulephera kukhala ndi zowayenereza kukhala m’dziko la South Africa.
A Chiponde apempha nzika za dziko lino kuti zizitsatira ndondomeko zonse zoyenelera zikamapita kunja kwa dziko lino monga kukhala ndi zikalata zoyendera zoyenerera.
Nzika zomwe zinabwera sabata yatha zinali zochokera m’maboma a Mzimba, Mangochi, Machinga ndi Balaka.