“Ma dotolo tilipo atatu, anamwino asanu koma patsiku timathandiza odwala kupitilira 3000”

Ogwira  ntchito pa chipatala chaching’ono cha Malomo m’boma la Ntchisi apempha boma kuti liwawonjezere ogwira ntchito pa malowo.

A Halima Daud kucheza ndi ogwira ntchito pachipatalachi

Chipatalachi chimafikira anthu opitilira 70,000 ozungulira derali mpaka kufikiranso mbali zina ndipo patsiku amathandiza anthu opitilira 3000.

Mmodzi wa mkulu woyang’anira pa chipatalachi a Zuze Khonde anawuza wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo a Halima Daudi omwe anayendera ntchito zomanga chipinda choyezelamo matenda osiyanasiyana pa chipatalachi.

Iwo anawuza ndunayi kuti kuchepa kwa ogwira ntchito pamalowo kwapangitsa kuti anthu odwala azichuluka ndiponso azilandila chithandizo mochedwa.

Iwo anena kuti madotolo pa chipatalachi alipo atatu okha, anamwino asanu ndi mmodzi, ogawa mankhwala mmodzi ndiponso oyesa matenda mmodzi omwe siwokwanila kuyelekeza ndi kuchuluka kwa anthu ofuna chithandizo.

Mkuyankha kwawo, Mayi Daudi ati ichi ndichimodzi mwa zifukwa zomwe boma likufuna kuwonjezera anthu ogwira ntchito mzipatala.

Iwo ati posachedwapa boma linalengeza kuti likufuna lilembe anthu ogwira ntchito mzipatala cholinga chofuna kuwonjezera anthu ogwira ntchito mmalo ngati cha Malomo.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Much awaited Judiciary complex expected to commence ‘soon’

The Judiciary says construction of its office complex in Lilongwe is expected to commence soon, as the procurement process is...

Close