Mlaka asusa mphekesera zoti akudwala mwakayakaya, akuti thupi latha chifukwa chosala kudya

Mmodzi wa oyimba nyimbo zauzimu, yemwenso ndi m’busa wa mpingo wa Fountain Gates Assembly, McDonald MlakaMaliro, watsutsa mphekesera zoti iwowa akudwala mwa kayakaya.

Kudzera mu program yomwe Times Radio imacheza ndi mbusayu ndi mkazi wawo Benadetta, iwo ati thupi lawo latha chifukwa cha kusala kudya osati nthenda ayi.

 

“Ndakhala ndikusala kuyambira chaka chatha mwezi wa July ndipo ndikadasalabe pa zomwe Mulungu anandiyankhula choncho ndati nditsutse zomwe anthu ena akufalitsa kuti ndikudwala mwa kayakaya,” iwo anatero.

 

Pakadali pano, iwo ali kunyumba yawo ku Balaka komwe kuli likulu la mpingo wawo.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
DPP Navicha defies Speaker: Refuses to respond to SONA in parliament, says she did already through media

Leader of Democratic Progressive Party (DPP) Mary Navicha has defied the direction given by the Speaker of Parliament Gotani Hara...

Close