Mlaka Maliro ang’alura Chakwera mu nyimbo: Ati ulendo wa ku Canaan sitikafika

Woyimba Mlaka Maliro akuti Malawi wasochera pa ulendo wake waku Canaan kotero sitikafika kamba koti ndodo yotisogolera yasowa.

A Maliro awuza atolankhani izizi atawafunsa kuti anenepo pa nyimbo yomwe ayimba koma sinatulusidwe kaye.

Mu nyimbo iyi, yotchedwa ndodo, a Maliro akuti: Yasowa, yasowa, yasowa mama ndodoya Moses. Ulendoopitaku Canaan, wavuta tikupita ku Libya. Mama yasowa! Ambuye okonda aliyense, akantheni anthu akubawa…”

Pulezidenti Lazarus Chakwera ndiwomwe analonjedza kuti utsogoleri wawo ukhala wa mkaka ndi uchi ngati ulendo wa ana Israel ku Canaan.

Poyankhula ndi atolankhani a Maliro anenetsa

kuti iwowo angofuna kuwawunikira a Malawi pa mmene dzikoli likuyendera.

Iwo anasindika kuti zomwe boma linalonjeza sizomwe zikuchitika.

“Basi yomwe takwera yasochera ndipo ku Canaan sitikafika,” atero a Mlaka.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Will DPP expel Jeffrey for failing to appear before disciplinary committee?

The Democratic Progressive Party (DPP) is still undecided whether to expel or suspend former secretary general, who is now Central...

Close