Mphunzitsi adya ndalama za mayeso za ophunzira 30, akanika kulemba mayeso
Ophunzira 30 pa sukulu ya sekondare ya Seven Hills pa Chimbiya ku Dedza salemba nawo mayeso a MANEB a Form 2 ndi Form 4 kaamba koti mphunzitsi wa mkulu pasukuluyi anawadyera ndalama zawo za mayeso .
Ena mwa ophunzirawa auza Zodiak kuti ndizokhumudwitsa kuti mtsogoleri wawo yemwe wawachita chipongwe.
Mwini wake wa sukukuyi a Hawa Ibrahim watsimikiza za nkhaniyi powonjezera kuti mphunzitsiyu anasakaza ndalama za ophunzira 20 ndipo khumi analephera kulipira ndalama ya mayeso.
Iwo ati nkhaniyi anakayitula ku polisi komanso analembera Kalata bungwe la MANEB ndipo anawauza kuti ndizosatheka kuti ophunzirawa alembe nawo mayeso a chaka chino.