Mutharika wasindika kuti akubweleranso kudzapulumutsa a Malawi ku chionongeko

Mtsogoleri wa chipani cha DPP a Peter Mutharika atsindika okha koyamba kuti dziko la Malawi lilibe utsogoleri ndipo iwo akubwelanso kuzapulumutsa a Malawi kuchiwonongeko.

“I, Peter Mutharika, am ready to lead DPP to victory again in 2025,” he says.

Iwo atinso pali anthu ena omwe akufuna kubweretsa lamulo loti iwo asadzayimile kamba ka zaka zawo. Koma mtsogoleri wa DPP-yu wati izi sizitheka ndipo iwo adzayimila chipani cha DPP m’chaka cha 2025.

A Mutharika akuyankhula izi pamsokhano wa atolankhani omwe ukuchitika kunyumba kwawo m’boma la Mangochi.

Mutharika atero: “Ndikuwawuza a Chakwera kuti sangatukule dziko lino pochita ndikulimbikitsa za zipolowe. Anthu akufuna utsogoleri osati nkhanza zanuzo. Nkhanzazo sizingathetse mavuto omwe Amalawi akukumana nawo pano monga njala komanso kusowa kwa ma passport.”

Iwo atinso kumenyedwa kwa otsatira chipani cha DPP mumzinda wa Lilongwe ndizomvetsa chisoni ndipo sizokufunika munthawi ya zipani zambiri.

A Mutharika afotokozanso kuti ndiwokhumudwa kuti chipani cha Malawi Congress (MCP) chikubweretsa ulamuliro wankhaza mdziko muno monga momwe zinaliri mu nthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi.

Iwo atsindika mfundo iyi potchula za kukhapidwa kwa otsatira chipanichi munzinda wa Lilongwe sabata ziwiri zapitazo.

Iwo atinso kuyambira lero kudzafika mwezi wa September chaka chamawa adzilankhula ndi Amalawi pafupipafupi pofuna kulimbikitsana nawo pa mavuto omwe akukumana nawo kamba kakulephela kwa boma.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
BWB stakeholders invest over 50,000 tree seedlings for 2024 forestry season of Mudi Catchment Area

Stakeholders in the private business sector, have contributed over 50,000 tree seedlings to Blantyre Water Board (BWB) for the restoration...

Close