Nankhumwa apempha boma liganizire omwe adasewerapo mpira wamiyendo ndi wa manja m’mbuyomu
Mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma m’nyumba ya malamulo a Kondwani Nankhumwa omwenso ndi phungu wa dera la Mulanje Central, apempha unduna woona za masewero kuti uganizire anthu omwe adasewerapo mpira wa miyendo komanso wa manja m’mbuyomu.

A Nankhumwa ati n’zomvetsa chisoni kuona a namandwa ena omwe adasewerapo mpira bwino m’mbuyomu akuvutika kwambiri.
Mwachitsanzo a Nankhumwa ati akatswiri ena omwe adasewerapo mpira m’mbuyomu akukhala moyo wovuta ndipo ena akuchita kusowa ndalama yoti apitire kuchipatala.
Nduna yoona za masewero a Uchizi Mkandawire yati unduna wawo ukukonza ndondomeko yomwe idzidzathandiza akatswiri osewera mpira opuma komanso omwe adathandizira ntchito za masewero kuti zipite patsogolo ndipo posachedwa, alengeza momwe ndondomekoyi idzigwilira ntchito.
Follow and Subscribe Nyasa TV :