Pulofeti awuza a Chakwera zofunika kuchita kuti chuma cha Malawi chiyende

Yemwe adayambitsa mpingo wa Life International Church, Prophet Amos Kambale, walangiza boma la a President Lazarus Chakwera kuti lileke kudalira thandizo lochokera mayiko akunja, koma kuti lipeze njira zomwe zingathandize potukula chuma cha dziko lino.

A Kambale adanena izi mu ulaliki wawo wolowera chaka chatsopano cha 2024. Mpingowu udakonza mapemphero antchezero pa sukulu ya Mbinzi mu mzinda wa Lilongwe.

“Nthawi yakwana tsopano kuti dziko la Malawi liyambe kugula makina ogwiritsa ntchito kumunda, ndipo makinawa aperekedwe kwa alimi akumidzi kuti adzilima ndi kukulora zambiri. Boma ligulenso makina a kompyuta ndi kugawa kwa achinyamata msukulu zosiyanasiyana,” adatero iwowa.

Mtumiki wa Mulunguyu adatsindikanso za kufunikira kolimbikitsa ntchito za migodi.

“Palibe dziko lomwe lidatukuka podalira thandizo lochokera mayiko ena. Palibe! Tikuyenera kupeza njira zomwe zingatithandize kukweza chuma chathu patokha, osati zomadalira thandizo la ena,” adatsindika a Kambale.

A Kambale adati ndi zochitiska chisoni kuti chuma cha dziko lino chikupitirirabe kulowa pansi, chikhalirenicho ngongole chitengereni ku mayiko ndi mabungwe osiyanasiyana.

Pa mapemphero amenewa, mtumiki wa Mulunguyu adachiritsa odwala matenda osiyanasiyana, osamva ndi akhungu.

Iwowo adaloseranso zambiri kwa akhristu omwe adapita kukapemphera ku mpingowu.

Kambale akuti amatenga chilimbikitso kuchokera kwa mlosi wa Mulungu wochokera mdziko la Zimbabwe an Emmanuel Makandiwa.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter

One reply on “Pulofeti awuza a Chakwera zofunika kuchita kuti chuma cha Malawi chiyende”

Comments are closed.