Sing’anga amangwidwa pobera mzimayi K125 000 atamunamiza kuti amachulukitsa ndalama

Ku Zomba, a Polisi amanga sing’anga wina waku Mozambique pomuganjizira kuti anabera mayi wina ponama kuti amachulukitsa ndalama.

M’neneri wa polisi ya Zomba, a Patricia Sipiliano ati sing’angayu ndi a Asima Abdul a dera la Lichinga mdziko la Mozambique.

A Sipiliano ati mayi wina, Linda Mfupika, anapita ku Chinamwali komwe anakumana ndi sing’angayu pa 3 April, chaka chino.

Ng’angayi akuti idauza a Mfupika kuti awapatse ndalama zokwanira K125,000 ponena kuti azichulukitsa. Kenako, Sing’angayu adauzanso mayiyo kuti supa zake zalephera kuchulutsa ndalamazo.

Apa mpamene mayiyu anakadandaula ku polisi ya Zomba ndipo apolisi anjata mkuluyu. A Asima Abdul akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu kuti akayankhe mlandu wakuba pogwiritsa ntchito upangiri wonama.

 

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
APM donates food stuffs to Muslims in Mangochi, vows he is standing and will win

Former President and Democratic Progressive Party (DPP) leader Peter Mutharika has maintained he will win next year’s presidential election as...

Close