Vuto la njala litha kusoneza zisankho mu 2025

Pali chiopsezo choti chiwerengero cha anthu odzavota pa anthu oposera 23,000 m’dera la Nsondole pansi pa mafumu a kulu Kuntumanji ndi Nkagula sadzavota nawo kutsala njala yamnanu m’boma la Zomba.

Malingana ndi anthu omwe tacheza nawo m’maderawa ati akungodya mango powaphika ngati ngosapsa penanso kupanga zokumwa powafinya akakhala opsera mumtengo ndipo izi zakhala zikuchitika kwa miyezi yoposera isanu (5).

A Gift Chiuma omwe ndi wokhudzidwa komanso Mfumu Sadi omwe dzina lawo lenileni ndi Louis Zgambo ati izi zili ndi kuthera kwakukulu kotenga miyoyo ya anthu ochuluka pomwe ena akumakomokakomoka kuphatikizapo anthu achikulire ndi ana.

Ndipo m’mawu ake yemwe akufuna kudzaimira uphungu m’derali a Leonard Kafunsila ati afikira kale mtsogoleri wa chipani cha People’s mai Joyce Banda ndipo akudikirira yakho ndipo iwo aperekapo thandizo lochepa la ufa.

“Ine kumbali yanga ndalakhulapo ndi mtsogoleri wa chipani chathu Mai Joice Banda ndipo andilonjeze kuti achitapo kathu”atero akafunsila.

Akafunsila atinso akumayendera anthuwa pa sabata lililonse kuti adziona umoyo wawo mmene ukuyendera.

Iwo ati kutalika kwa mtunda wokapeza nthandizo la zipangizo za ulimi zotsika mtengo (AIP) ndi zinanso zomwe zakoledzera vutoli,ponena kuti anthu ena akumayenda mtunda wa makilomita 3 enanso mpaka 10 kuti akapeze zipangizozi,zomwe nzosowekera mphamvu pokudyanso mukwanira.

“Vutoli kumbali ina yakula potengeranso kuti dziko lino linakhudzika ndi namondwe nde anthu ambiri sanadzitolerebe komanso kupeza katundu mu AIP mtunda ukukhala wautali kwa anthuwa madela amenewa, ndipo pakufunika mphamvu zoyendera kukafika ku malowa koma zingatheke ndi chakudya chokha basi” Anaonjezera motero akafunsila.

Tinayesetsanso kuti tiyakhule ndi phungu yemwe akuimira derali a MacNice Abu Naliwa koma foni yawo simapezeka.

Naliwa ndi phungu wa chipani cha Democratic Progressive(DPP) ndipo izi a Kafunsila akufuna kuti adzaimire mpando omwewu pansi pa chipani cha People’s (PP).

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Kabambe not happy with UTM followers continued loyalty to Usi: Will UTM unite?

The United Transformation Movement (UTM) appears to be facing a profound internal crisis as newly-elected leader Dalitso Kabambe is reportedly...

Close