A Alex Major, omwe anachosedwa mu MCP, adzudzula MCP podzudzula DPP

Mmodzi mwa anthu omwe anachotsedwa mchipani cha Malawi Congress Party-MCP Alex Major wati zomwe apanga achipanichi podzudzula DPP pochotsa anthu ena ‘ndizogwetsa ulesi’.

Major anachotsedwa mchipani cha MCP mu 2022 ponena kuti samalemekeza mfundo zamtsogoleri wawo Lazarus Chakwera.

Poyankhula ndi Nyasatimes, Major wati ndizoseketsa kwambiri pakalata yomwe atulutsa a MCP kamba koti iyeyo anachotsedwa atangolembeledwa kalata ndi Mlembi wawo Eisenhower Mkaka koma sanapite kunthambi yolimbikitsa mwambo.

Malingana ndi Major,  akukhulupilira kuti kalatayi yalembedwa ndi anthu ochepa osati akulu akulu onse achipani cha MCP kamba koti paokha amalalikira zaumodzi koma mchipanimo mulibenso zimenezo.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter