Bushiri apitiliza ntchito yogawa chakudya: Pano wafika ku Nsanje

Shepherd Bushiri wapereka thandizo la chakudya kwa anthu omwe akhala akukhudziwa ndi njala kwa mfumu yaikulu Mbenje m’boma la Nsanje.

Izi zinatsatira maripoti oti anthu ku delari akhala akudya zakudya monga nyika komanso zikhawo pofuna kupewa imfa ndi njala.

Mchitidwe wu, unapangitanso kuti anthu ena akumane ndi ngozi zina kuphatikizapo kulumidwa ndi n’gona.

Ndipo polankhula ndi mkulu wina otchedwa Fanuel Benda yemwe mkazi wake anaphedwa ndi n’gona, Bushiri anati ndi okhudzidwa ndi mavuto omwe anthuwa akukumana nawo.

Bushiri, wati apitiriza kuthandiza anthu omwe akukhudziwa ndi njala.

“Ino ndi nthawi yomwe tonse tikuyenera tithandizane wina ndi nzake. Aliyense atengepo gawo, “anatero Bushiri.

Kufikira pano, Bushiri wathandiza anthu mmaboma a Ntcheu, Mulanje, Thyolo, Zomba, Lilongwe, Nkhatabay, Mzimba ndi Nsanje

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
CARE to launch new business strategy meant to reshape lives of over 3.5 million people

CARE International in Malawi is this Thursday unveiling a transformative Business Plan poised to reshape the lives of over 3.5...

Close