Chipani cha UTM chidzudzula a polisi polephera kumanga anthu anayambisa ziwembu ku Lilongwe

Chipani cha UTM chadzudzula nthambi zachitetezo ati kamba kolephela kumanga anthu amene amapanga zachiwembuzo.

Chilima

Chipanichi chadzudzulanso mchitidwe wa zipolowe omwe anthu ena anachitira otsatira chipani cha DPP dzulo ku Lilongwe.

Kudzela mu kalata yomwe wasainira ndi mneneri wake Felix Njawala, UTM yati ndale zomaophyezana ndizachikale komanso zilibe malo mu ulamuliro wa demokalase.

Chipani cha UTM chati sichipanga nawo ndale za ziwawa.

Dzulo chipani cha DPP chinakonza mwambo wa mdipiti wa galimoto (motor parade) kuzungulira mu mzinda wa Lilongwe pofuna kudziwitsa anthu za mbili za chipanicho.

Koma mwadzidzi, anthu ena anayamba kugenda miyala galimoto zimene zinali pa mdipitiwu.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
MALGA responds to budget, says its not ‘inspiring’ fiscal devolution to councils

Malawi Local Government Association (MALGA)—an umbrella body of all local government authorities—has said the proposed 2024/2025 national budget is not...

Close