Francis Berekanyama apereka mphoto zokwana K6Million kwa osewera mpira ochita bwino mu Berekanyama Trophy

Kudali kusangalala, kululutira pa Matsimbe Primary School mdela la mfumu yaikulu Masula pamene phungu wadelaro Francis Berekanyama amapereka mphoto kwa achinyamata mdelalo omwe achita bwino pampikisano wa Berekanyama Trophy.

Mukulankhula kwawo a Berekanyama adayamika achinyamata kamba koonetsa luso pankhani ya zamasewero.

Pamwambowo, Mneneli wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Ezekiel Peter Ching’oma, adayamika a Berekanyama kamba kokhadzikitsa chikho chimenecho.

A Ching’oma adawuza otsatira chipanichi kuti atakhala pansi ku komiti yaikulu ya chipanichi (NEC) adagwirizana kuti Chakwera ndi amene ataimire chipanichi pamasankho akulu a 2025.

Iwo adati Chakwera akuyenera kupitiliza kulamula kamba koti mu ulamuliro wawo akumana ndi mabvuto ochuluka choncho akuyenera kupitiliza kukonza zinthu.

Mukulankhula kwawo , wapampando wa chipani cha Malawi Congress (MCP) mchigawo cha pakati a Patrick Zebron Chilondola adayamikira mtsogoleri wadziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera kamba koti ndi mtsogoleri yekhayo yemwe waonetsa chidwi pankhani zotukula dziko lino.

Iwo adati pa chifukwachi, a Chilondola apempha a Malawi kuti asagwedezeke.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
DPP Wrangles Continue, as Nankhumwa Closing Remarks in Parliament hijacked

Leader of Opposition Kondwani Nankhumwa failed to make closing remarks to Parliament on Friday, after Speaker Catherine Gotani Hara first...

Close