Kawale apempha a Malawi kuti alimbikire ulimi wothirira chifukwa ng’amba yafikapo

Nduna yoona za malimidwe a Sam Kawale yapempha anthu m’dziko lino kuti ayambe kupanga ulimi wamthilira pofuna kupewa njala pomwe ng’amba yafika posauzana mdziko muno.

A Kawale amayankhula izi pomwe amakhazikitsa ntchito yogawa ufa ku maanja omwe akhudzika ndi njala kwa Msakambewa m’boma la Dowa.

Iwo ati boma layika ndalama zambiri ku unduna wa za malimidwe pofuna kuthetsa njala mdziko lino.

Mfumu yayikulu Msakambewa yayamikira boma kaamba kobweretsa thandizoli munthawi yake koma yapempha adindo kuti awonjezere chiwerengero cha anthu amene akulandira thandizoli mderali.

Maanja okwana 29, 333 ndi amene alandire thandizo la ufali m’boma la Dowa.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Catholic Bishops issues pastoral letter: Blames voters for choosing leaders who can’t govern

The Episcopal Conference of Malawi-ECM says voters are to blame for choosing leaders who can't govern properly though it also...

Close