Mnyamata wa zaka 17 azipha poziwombera ndi mfuti kamba kosemphana ndi chibwezi chake
Mnyamata wa zaka 17 Tinasha Mtawali, wadzipha ku Chitipi m’boma la Lilongwe, pa nkhani zomwe zikuganizilidwa kuti ndi za chibwenzi.
Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu wati mnyamatayu adaimbira lamya chibwenzi chake kuchiuza kuti sadzamuonanso.
A Chigalu ati ali mkati molankhulana, bwenzi lakelo linamva kuombedwa kwa mfuti ndipo Tinasha adaleka kulankhura.
Izi zidapangitsa bwenzi lakelo kudziwitsa abale a Tinasha za izi.
“Bambo a malemu Tinasha adasakasaka mfuti yawo mnyumba atamva za izi ndipo adapeza kuti yasowa. Pamodzi ndi apolisi adayamba kusaka Tinasha, yemwe wapezeka atafa dzulo ku Chitipi, mfuti ili mmanja komanso lamya yake ili pambali pake,” atero a Chigalu.
Malemu Tinasha amachokera mmudzi mwa Likuzi, mfumu yaikulu Sezani m’boma la Ntcheu
Follow and Subscribe Nyasa TV :