Mulandu wa malemu Wittika: Khoti likumanaso lachiwiri mulungu wa mawa

Oweruza milandu Mzonde Mvula wayamba wayimitsa kaye kumva mlandu wa a Lester Maganga omwe akuwaganizira kuti anapha a Allan Witika mpakana pa 9 April chaka chino.

Izi zili chomwechi chifukwa choti mboni ziwiri zaboma zomwe zimayenera kupelekera umboni sizinabwere.

Bwaloli limayembekezeka kupitiliza kumva mlanduwu kuyambira lero kufikira lachinayi sabata ino.

A Mvula atinso adzadziwitsa pa nthawi yoyikila maloya a boma komanso a Maganga pa chigamulo chawo pa pempho loti a Maganga awatulutse pa belo.

Mwazina, bwaloli linapeleka mwayi kwa atolankhani kuti aone nawo umboni wa kanema ya chisisi (CCTV) yomwe imaonetsa munthu yemwe anavala malaya ofiyiyira, yemwe mboni yachi khumi yaboma a Paulo Mvula inati ndi omwe anamuona ali pa foni m’galimoto lomwe mudapezeka thupi la a Witika.

Masiku onse omwe a Maganga akhala akulowa m’bwaloli amavala suti koma lero anavala thalauza la jeans ndi malaya oyera zomwe zidapangitsa a Mvula kufunsa: “Bwanji lero simunavale suti.”

Ndipo a Maganga anati ma suti  awo onse mngakuda.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
1 Comment
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
James
James
1 month ago

Ma loyal, Khoti…. Chichewa chakuti ichi

Read previous post:
High Court rebuffs Chilima: Says it’s premature to seek disclosures as they are sensitive

The High Court in Lilongwe has today ruled that it is premature for the defence in Vice President Saulos Chilima's...

Close