Pakali pano tafikira anthu oposa 700 000 ndi chimanga chaulere, atero Bushiri

Prophet Shepherd Bushiri wati pakali pano ntchito yawo yogawa chimanga chaulere kwa a Malawi omwe akhuzidwa ndi ngozi zadzidzidzi yikupitilirabe ndipo panopa afikira anthu oposa 700 000.

Kusakala: Tafikira anthu oposa 700 000

Mneneri wa a Bushiri a Aubrey Kusakala anena izi ku Mangochi komwe athandiza mabanja oposa 200 mdera la Senior Chief Nankumba ku Monkey-Bay m’boma la Mangochi.

A Bushiri achita potsatira vuto lakusefukira kwa madzi lomwe lakhudza mabanja ankhaninkhani maka mbali mwanyanja mdziko muno.

Mneneri wa a Bushiri a Aubrey Kusakala ati potsatira vuto lomwe linagwera anthuwa, mmneneriyu anaganiza zothandiza anthuwa.

A Kusakala ati aka ndi kachitatu kugawa chimanga ku Mangochi ndipo pakadali pano ntchito yogawa chimanga chaulere ya chaka chino kwa anthu osowa mdziko muno yafikira anthu oposa 700,000.

Anthu ammaboma a Karonga, Nkhotakota, mzinda wa Mzuzu, Nkhatabay, Ntcheu Lilongwe, Nsanje, Mulanje, Thyolo ndi Zomba ndi omwe alandira nawo thandizoli.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter