Alimi a fodya adandaula ati sakulandirabe ndalama zawo ngakhale anagulisa fodya kalekale

Alimi a fodya omwe anagulitsa fodya wao sabata loyamba la msika wafodya adandaula kuti sanalandirebe ndalama zawo pomwe msika walowa sabata yachiwiri.

Mmodzi mwa alimiwa a Msaiwale Zakaliya omwe analinso ndi anzawo ena oposa khumi aku Chamama m’boma la Kasungu ati ali kakasi chifukwa adatumiza msanga fodya kuti atumize ana ku sukulu.

Iwo ati malamulo amati alimi azilipidwa ndalama mmaora 24 asanadutse akagulitsa fodya wao koma akuluakulu a msika wafodya akuti sakulongosola chomwe chachedwetsa ndalamazi.

Mneneri wa bungwe la Tobacco Commission, Telephorus Chigwenembe wati bungweli linali lisanalandire dandaulo pankhaniyi ndipo alonjeza kuti afufuza ndikulumikizana ndi mbali zokhidzidwa kuti adziwe chomwe chachititsa izi.

Mkulu woona za fodya ku Kampani ya AHL group a Graham Kunimba anati tiwatumizire mafunso olemba kuti ayankhepo pa nkhaniyi omwe Zodiak yawatumizira.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Pakali pano tafikira anthu oposa 700 000 ndi chimanga chaulere, atero Bushiri

Prophet Shepherd Bushiri wati pakali pano ntchito yawo yogawa chimanga chaulere kwa a Malawi omwe akhuzidwa ndi ngozi zadzidzidzi yikupitilirabe...

Close