Watulukira Gaddafi General Longwe! Akuti muvoteleni kuti a Malawi mulawe kusintha

Mzika ya dziko lino a Eddie Gaddafi General Longwe omwe amakhala mdziko la Asia ati alindichidwi chopikisana nawo pazisankho za mtsogoleri wadziko lino zomwe zikuyembekezeka kuchitika chaka chamawa ngati oyima pawokha.

Gadafi

Agadafi auza Nyasatimes kuti iwo ndiwokonzeka kuombola amalawi omwe pakadali pano akukumana ndimavuto osiyanasiyana mu ulamuliro wa presidenti Dr. Lazarus Chakwera.

Iwo ati ali ndinfundo zikuluzikulu zingapo zomwe akuti ndizothandiza kutukula dziko lino komaso miyoyo ya amalawi.

Zina mwamfundozi ndimonga kuthana ndikatangale, kulimbikitsa nkhani za ulimi ndikuti dziko lino likhale ndichakudya chokwanira, kulimbikitsa olamuliro wabwino, kulimbitsa chitetezo cha dziko komanso kutukula ntchito za umoyo m’magawo osiyanasiyana.

“Pali zambiri zomwe ndakonzekera kuwachitira amalawi anzanga. Azuzika kokwana ndipo nthawi yoti awomboledwe yakwana,” watero Longwe.

Kotero iye wapempha anthu kuti adzamuvotere mwa unyinji kuti masomphenya ake azakwanilitsidwe maka ofuna kutukula dziko lino.

Longwe anabadwira ndikukulira mchigawo chakumpoto kwadziko lino.

Bambo ake amachokera m’boma la Nkhotakota pomwe mayi ake amachoka m’boma la Mzimba.

Kunkhani zamaphunziro, Longwe ali ndi digli ya za business komaso diploma yokhudza makompyuta.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
2 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
Wilfred Ngwira
Wilfred Ngwira
3 months ago

Trying your best is not a sin

Noname
Noname
3 months ago

Dziko la Asia?

Read previous post:
Govt upbeat about economy: Expects gradual recovery with 3.2% growth in 2024

Minister of Finance and Economic Affairs, Simplex Chithyola Banda, says the government expects to register gradual economic recovery with a...

Close