Zachitikanso ku Dedza: Bambo amenya mkazi wake mpaka kufa
Patangodusa mwezi umodzi pomwe bamboo wina anawombera mkazi mpaka imfa ku Dedza, thambo lakuda lagwanso mubomali pomwe mayi wina m’mudzi mwa Yahaya pa boma ku Dedza wafa atamenyedwa ndi mamuna wake.
Mfumu Yahaya yauza Nyasatimes kuti mayiyu ndi mamuna wake onse anali ku mowa dzulo koma anayamba kukangana kumeneko kamba koti mkazi wake amalankhula ndi amuna ena.
A Yahaya ati nkangano wa awiriwa unapitilira ndipo atakafika ku nyumba yawo bamboyu anamenya mkazi wakeyu mwa nkhaza.
Anthu okwiya m’mawa uno amafuna aphe bamboyu ndipo apolisi anathira utsi okhetsa msozi kubalalitsa anthuwa,pakali pano bamboyu amutengera kupolisi.
Thupi la mayiyu tsopano lili ku nyumba ya chisoni pa chipatala chachikulu cha Dedza.
Follow and Subscribe Nyasa TV :