Anthu asanu ndi mmodzi amwalira, ambiri avulala pa ngozi ya ku By-pass ku Lilongwe

Zachitika ku msewu wa By-Pass ku Lilongwe komwe anthu asanu ndi mmodzi amwalira ndipo ena atatu avulala modetsa nkhawa pangozi ziwiri zomwe zachitikira malo amodzi.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu wati Lamulungu, galimoto ya mtundu wa truck ya kampani ya Central Poultry inali itafa, kotero inangoima pa msewu.

Cha ma 7 koloko madzulo, galimoto ya mtundu wa lorry inanyamula anthu 21 kuchokera mbali ya Zamkutu, ndipo itatafika pa malopo, galimotoyo inaomba kumbuyo kwa galimoto yoonongekayo.

A Chigalu ati apa, munthu m’modzi yemwe anali ku tsogolo anavulala m’mutu ndi miyendo ndipo anakamwalira ku chipatala cha Kamuzu Central.

Iwo ati anthu ali mkati mothandiza kupulumutsa ovulala, kunabweranso galimoto ya mtundu wa Mazda Axela yomwe inaombapo anthu anayi kuphatikiza dalaivala wa truck, omwe anavulala.

Atapita nawo ku chipatala, dalaivala wa Axela a Kesswell Munthali, dalaivala wa truck komanso anthu ena atatu omwe anaombedwa anamwalira, kubweretsa chiwerengero cha anthu omwalira pa asanu ndi mmodzi.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Emmie Deebo to perform at Zanzibar International Youth Summit

The fastest rising female musician Emmie Deebo has been booked to perform and represent Malawi at the Zanzibar International Youth...

Close