Chakwera adzudzula boma la USA poletsa a Malawi ena kupita ku USA: ‘Akuzengedwa milandu, khoti silidawapezebe olakwa.’

President Lazarus Chakwera wati ndiodabwa ndi ganizo la dziko la America loletsa mzika zinayi zadzikolino kupita mdzikoli ati kamba kokhudzidwa ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale.

Mtsogoleriyu wati ndizodabwitsa kuti dziko la America likupeleka chilango kwa anthu omwe bwalo lamilandu kuno silidawapeze olakwa chikhalirecho ku America ko kumachitika umbava ndi umbanda ochuluka kuposa ku Malawi kuno.

A Chakwera adzudzulanso mchitidwe wa anthu ena a mdzikolino omwe amalimbikitsa kufalitsa nkhani zoipa za dzikolino ku maiko akunja. Iwo ati pali zambiri zabwino zomwe Malawi yachita mmagawo monga olimbana ndi ziphuphu ndi katangale.

Iwo amalankhula izi lero ku Lilongwe pamsonkhano otsegulira zokambirana zopititsa patsogolo chuma cha dzikolino kudzera mu ulimi, ntchito zokopa alendo komanso migodi.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Lake Malawi lakeshore floods: Govt tells of affected developers, says ‘You are negligent’.

The National Water Resource Authority (NWRA) is attributing the current flooding disaster along the lakeshores to negligence among developers. According...

Close