Navicha adzudzula Chakwera: Palibe chachilendo, angobwereza malankhulidwe

A Mary Navicha omwe chipani cha DPP chawasankha kukhala mtsogoleri wa zipani zotsutsa mnyumbayi ati zomwe Pulezidenti Lazarus Chakwera walankhula palibe chachilendo angobwereza malankhulidwe awo okoma koma kukanika kuchita.

Mary Navicha

Polankhula masanawa ku nyumba ya malamulo a Navicha ati iwo ndiokonzeka kumenyera nkhondo a Malawi powonetsetsa kuti zomwe mtsogoleri-yi walankhula akwaniritse kupanda apo atule pansi udindo potengera zomwe anauza a Malawi mbuyomu.

 

A Navicha ati chipani cha DPP chakonzeka kulankhulapo mnyumbayi sabata ya mawa pa zomwe mtsogoleri-yu walankhula pa m’mene zinthu zilili mdziko lino. Ndipo ati iwo adzalankhula ngati mtsogoleri wa zipani zotsutsa mnyumbayi.

 

Pa zomwe Sipika wanena kuti a Nankhumwa ndi omwe akuwavomereza padakali pano ngati mtsogoleri wa zipani zotsutsa, a Navicha ati mtsogoleri wa zipani zotsutsa amakhala m’modzi ndipo malingana ndi malamulo amnyumbayi DPP ndi yomwe ikuyenera kusankha mtsogoleri-yu.

 

” Sindiyankhula zambiri tingodikira timve kuti mlangizi waboma pa nkhani zamalamulo apeleka langizo lotani kwa a Sipika,” anatero a Navicha.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
National Planning Commission reacts to Chakwera’s SONA: “This is the most MW-2063 centric SONA.”

The National Planning Commission (NPC) says President Lazarus Chakwera’s State of Nation Address (SONA) is the substantially geared to achieving...

Close