Vuto la ma pasipoti lizatha? A Zikhale akuti makina alipowo akuchedwa, akupanga mapasipoti 500 okha pa tsiku

Nduna yoona za m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma yati makina amene akuwagwiritsa ntchito posindikiza ziphaso zoyendera (passports) akugwira ntchitoyo mochedwa kwambiri.

Ndunayi yati makinawa akumasindikiza ziphaso zosadutsa 500 patsiku zimene zikuchititsa ntchitoyi kumagwirika mochedwa.

Iwo ati pakadali pano nthambiyi ili ndi ziphaso zofuna kusindikiza zokwana 35,000 zimene ikudikira koma apereka chikhulupiriro kuti izi zitheka posachedwapa.

A Ng’oma anena izi pamene adakayendera likulu la nthambiyi mu mzinda wa Blantyre.

Iwo ati adapeza kampani ina ya m’dziko momwe muno imene yakhala ikugwira ntchitoyi pamene akudikira kupeza ina yoti izigwira ntchitoyi mokhazikika.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Historical! Malawi opens diplomatic relation with Israel, MOU on labour export deal signed

Malawi Embassy in Tel Viv, Israel, has officially been opened today with a blessing of also having the memorandum of...

Close