Wapolisi azipha poziponya munsinje kamba ka chibwezi

 

Wapolisi wina ku Rumphi wadziponya mu mtsinje wa South Rukulu omwe pano wadzadza ndikusefukira mbali zina m’bomali.

Mneneri wa polisi mchigawo chakumpoto a Maurice Chapola, angotsimikiza zoti alandira lipoti lakusowa kwa a Ngamanya Mbale koma anakana kuyankhulapo zambiri ponena kuti kafukufuku wawo ali mkati.

Koma yemwe watitsina khutu wati a Mbale adziponya mu mtsinjewu atakangana ndi mkulu wina pa nkhani zokhudza chibwenzi.

Wapolisiyu akuti anamenyana ndi mkuluyu zinthu zomwe zinachitsa mtsikana yemwe amakanganirana kuyitanitsa apolisi anzake kudzalanditsa ndewu koma anapeza itatha.

Yemwe watitsana khutu wati wapolisiyu anapita ku malo ena okopa alendo m’bomali komwe amayankhula kwa anzake ena kuti adziponya mu mtsinje, kenano anasowa osawonekanso.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Anarchy won’t print passports, Mutharika dares Chakwera on political violence

Democratic Progressive Party (DPP) president Peter Mutharika has blamed the Malawi Congress Party for the violence that happened at Mbowe...

Close