Chakwera apempha Amalawi kuti achilimike pa ntchito yotukula dziko

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera wapempha Amalawi kuti achilimike pa ntchito yotukula madera awo posadalira kuti ena adzawagwirire ntchitoyo.

Chakwera anena mauwa m’boma la Nkhata Bay Lamulungu pamwambo wokumbukira omwe adaphedwa ndi azungu pomenyera ufulu wa dziko lino.

Iwo adati Amalawi ayenera kuphunzira kwa ‘makolo athu’ omwe adagwiritsa ntchito zipangizo zomwe zidalipo pomenyana ndi azungu.

“Azungu a ku Southern Rhodesia atamva kuti makolo athu abvuta kuno ku Nkhata Bay, anatumiza akasinja, galimoto zankhondo kuti azathane nawo, ndipo anthu aku Chitipa atamva zimenezi anayamba kuyika mitengo mmiseu kuti galimotozo zisadutse. Iwo saanalole kuti kusapezeka kwa mifuti ndi zida zina zomenyera ufulu wathu kuwalepheretse kugwiritsa ntchito zipangizo zomwe analinazo. Ndiye ifenso pofuna kuthana ndi umphawi omwe wadzadza mdziko muno, tiyeni tichirimike pogwiritsa ntchito zida ndi nzeru zomwe tiri nazo,” anatero mtsogoleriyu.

Chakwera anatinso amalitili omwe adafera ufulu wa dziko lino adawonetseranso kuti mzika yabwino siilola kuti anthu akunja azidyera masuku pamutu pa eni dziko.

Iwo anati ndi zachisoni kuti ngakhale adali atakhala mdziko muno kwa zaka makumi asanu (50), iwo anali osakhutitsidwabe ndi ukayidi wa Amalawi.

“Mu chaka cha 1953 atsamundawo anapanga chiganizo chophatikiza dziko lathu ku Federation la Rhodesia, lomwe linali ndi utsogoleri wa nkhanza. Tsiku limenelo ndilimene makolo athu ananena kuti enough is enough. Tsiku limenelo ndilimene makolo athu anaona kuti munthu wakunja saafunika kumulora akubere chuma chako. Ndipo nthawi imeneyo zinafika poti mMalawi aliyense amene atapezeke akucheza ndi atsamunda amasalidwa kuti ameneyo ndi Kapirikoni, munthu ogulitsa dziko lake lomwe. Ndiye posangalala ndi chitsanzo chimenechi, nafenso tiyenela kuzindikira kuti ena obwera mdziko muno,” a Chakwera adatero.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Education activists excited with MK900bn budget allocation to the sector

The Civil Society Education Coalition (CSEC) has commended the government for allocating MK900 billion to the education sector in the 2024-2025...

Close